47 Aisiraeli onse m’masiku a Zerubabele+ komanso m’masiku a Nehemiya+ anali kupereka gawo loyenera kwa oimba+ ndi alonda a pachipata+ malinga ndi zofunikira zawo za tsiku ndi tsiku. Ndipo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa Alevi.+ Aleviwo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa ana a Aroni.