5 Eliyasibu anakonzera Tobia chipinda chachikulu chodyeramo+ m’chipinda chimene nthawi zonse anali kuikamo nsembe yambewu,+ lubani, ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda a pazipata anayenera kulandira, komanso zimene anali kupereka kwa ansembe.