26 Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli?+ Mwa mitundu yonse panalibe mfumu yofanana naye.+ Iye anakondedwa ndi Mulungu wake,+ mwakuti Mulungu anamuika kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Koma akazi achilendo anamuchimwitsa.+