3 Kuwonjezera pamenepo, Esitere analankhulanso ndi mfumu ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamapazi a mfumuyo. Iye analira+ ndi kuchonderera kuti mfumu imukomere mtima. Ndiponso kuti isinthe choipa+ cha Hamani Mwagagi ndi chiwembu+ chimene anakonzera Ayuda.+