-
Esitere 8:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Tsopano Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima,+ komanso ngati n’zoyenera kwa inu mfumu ndiponso ngati ndine munthu wabwino kwa inu, palembedwe makalata ofafaniza makalata+ achiwembu amene Hamani, mwana wa Hamedata Mwagagi,+ analemba pofuna kuwononga Ayuda+ amene ali m’zigawo zanu zonse mfumu.+
-