3 “Monga mtengo wa maapozi+ pakati pa mitengo ya m’nkhalango, ndi mmene alili wachikondi wanga pakati pa ana aamuna.+ Ineyo ndinali kulakalaka mthunzi wa wokondedwa wanga ndipo ndinakhala pansi, pamthunzi wakewo. Chipatso chake chinali chotsekemera m’kamwa mwanga.