6 Choncho iweyo upite kukawerenga mokweza mawu a mumpukutu. Ukawerenge mawu amene walembamo, mawu a Yehova+ amene ndakuuza. Ukawerenge mokweza pamaso pa anthu onse m’nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya.+ Ukawerengenso pamaso pa anthu onse a ku Yuda amene akubwera kuchokera m’mizinda yawo.+