23 Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, Yehudi akawerenga zigawo zitatu kapena zinayi za mpukutuwo, mfumu inali kudula mpukutuwo ndi mpeni wa mlembi ndi kuponya chidutswacho pamoto umene unali mumbaula. Inachita izi kufikira mpukutu wonsewo itauponya pamotopo.+