30 Choncho ponena za chilango chimene adzapatsa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sipadzapezeka mwana wake aliyense wokhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mtembo wake adzautaya kunja+ kumene udzakhala padzuwa lotentha masana ndipo usiku udzakhala kunja kozizira.