4 Ndiyeno Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse ankhondo ataona adaniwo anayamba kuthawira+ kunja kwa mzinda usiku. Iwo analowera njira ya kumunda wa mfumu,+ kukatulukira pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, n’kupitiriza kuthawa molowera ku Araba.+