20 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi zovala za m’mikono za akazi inu, zimene mukukolera miyoyo ya anthu ngati kuti ndi mbalame. Ine ndizichotsa m’mikono mwanu ndi kumasula miyoyo ya anthu imene mukuikola ngati mbalame.+