32 “‘Zimenezi zidzamuchitikira chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo.+ Farao ndi khamu lake lonse adzaikidwa m’manda pakati pa anthu osadulidwa. Iye adzaikidwa m’manda pamodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”