6 “‘Chotero pali ine Mulungu wamoyo, mlandu wa magazi udzakutsatira chifukwa ndinakonza zoti magazi ako akhetsedwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Ndithudi iwe unadana ndi amene unakhetsa magazi awo, choncho mlandu wa magazi udzakutsatira.+