-
Ezekieli 40:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Kenako anafika pachipata chimene chinayang’ana kum’mawa+ ndipo anakwera pamasitepe ake. Pamenepo iye anayamba kuyeza malo apafupi ndi khomo la kanyumba ka pachipatako+ ndipo anapeza kuti malowo anali bango limodzi m’lifupi. Malo apafupi ndi khomo la mbali ina ya kanyumbako analinso bango limodzi m’lifupi mwake.
-