22 Miyezo ya mawindo ake, khonde lake ndi zithunzi zake za mtengo wa kanjedza,+ inali yofanana ndi miyezo ya zinthu zomwezi za kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kum’mawa. Anthu akafuna kulowa m’kanyumbako anali kukwera masitepe 7, ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa anthuwo.