58 Mwachitsanzo, pamene wokusumira mlandu akupita nawe kwa wolamulira, yesetsa kuchitapo kanthu muli m’njira, kuti uthetse mlanduwo. Uchitepo kanthu kuti asakutengere kwa woweruza, ndi kutinso woweruzayo asakupereke kwa msilikali wa pakhoti, ndipo msilikaliyo n’kukuponya m’ndende.+