10 Popeza Chilamulo ndicho mthunzi chabe+ wa zinthu zabwino zimene zikubwera osati zinthu zenizenizo, ndiye kuti anthu wamba sangachititse anthu amene amalambira Mulungu kukhala angwiro. Iwo sangathe kuchita zimenezi mwa nsembe zimodzimodzizo zimene amapereka mosalekeza chaka ndi chaka.+