Mawu Akumapeto
^ [1] (ndime 14) N’zoona kuti pali zambiri zimene zimafanana pakati pa ukapolo wa zaka 70 umene Ayuda anakhala ku Babulo ndi zimene zinachitikira Akhristu odzozedwa. Komabe sitinganene kuti ukapolo wa Ayuda unkaimira zimene zinachitikira Akhristuwa. Choncho si bwino kuganiza kuti chilichonse chimene chinachitika ku ukapolo wa Ayuda chinakwaniritsidwanso pa Akhristu. Pali zina zimene zikusiyana. Mwachitsanzo, ukapolo wa Ayuda unali wa zaka 70 koma wa Akhristu unali wa nthawi yaitali kuposa pamenepa.