Mawu a M'munsi
Pambuyo potchula “Efuraimu,” Baibulo la Septuagint limawonjezera mayina ena asanu, pamene limati: “Koma Manase anali ndi ana ndipo wina anali Makiri, amene mdzakazi wake wa ku Siriya anam’berekera. Ndipo Makiri anabereka Galaadi. Koma ana a Efuraimu, m’bale wake wa Manase, anali Sutalaamu ndi Taamu. Sutalaamu anali ndi ana ndipo wina anali Edemu.” Ichi chingakhale chifukwa chake Baibulo la Septuagint limatchula anthu 75 m’malo mwa 70 pa Ge 46:27 ndi pa Eks 1:5, komanso Sitefano anatchula zomwezi pa Mac 7:14.