Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO

Mawu a M'munsi

a M’kulakalaka kwawo kubweranso kwa Yesu, Mboni za Yehova zinapereka madeti amene sanali olondola. Chifukwa cha zimenezi, ena amawatcha aneneri onyenga. Komabe, palibe mpamodzi pomwe m’zochitika zimenezi pamene ananena kuti maulosi amenewo anawanena ‘m’dzina la Yehova.’ Iwo sananene konse kuti, ‘Awa ndimawu a Yehova.’ Nsanja ya Olonda, magazini alamulo a Mboni za Yehova, inanena kuti: “Tilibe mphatso ya kunenera.” (January 1883, tsamba 425) “Ndiponso sitidzalola kuti zolembedwa zathu zilambiridwe kapena kulingaliridwa kukhala zosalakwa.” (December 15, 1896, tsamba 306) Nsanja ya Olonda inanenanso kuti chenicheni chakuti ena ali ndi mzimu wa Yehova “sichimatanthauza kuti amene akutumikira tsopano monga mboni za Yehova ali ouziridwa. Sizimatanthauza kuti zolembedwa m’magazini ano a Nsanja ya Olonda nzouziridwa ndi zosalakwa ndi zopanda zophophonya.” (May 15, 1947, tsamba 157) “Nsanja ya Olonda simanena kuti ndimawu ouziridwa, ndiponso siili yaukumu.” (August 15, 1950, tsamba 263) “Abale amene amakonza mabuku ameneŵa sali osakhoza kulakwa. Zolemba zawo sizili zouziridwa mofanana ndi zija za Paulo ndi olemba Baibulo ena. (2 Tim. 3:16) Ndipo chotero, nthaŵi zina, kwakhala kofunika kuwongolera malingaliro ena, pamene chowonadi chinamvekera. (Miy. 4:18)”—February 15, 1981, tsamba 19.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena