Mawu a M'munsi
a Kelvin ndi mlingo wa muyeso wa temperecha umene madigiri ake afanana ndi madigiri a muyeso wa temperecha wa Celsius, kokha kuti muyeso wa temperecha wa Kelvin umayambira pa absolute zero, kutanthauza 0° K—yolingana ndi -273.16 digiri Celsius. Madzi amaundana pa 273.16 K ndipo amaŵira pa 373.16 K.