Mawu a M'munsi
b Zitsogozo za mu 1995 zimagwira ntchito kwa misinkhu yambiri koma osati yonse. “Ambiri akuvomereza kuti zitsogozo zatsopano za kulemera kwa thupi sizikugwira ntchito kwa anthu azaka zoposa 65,” akutero Dr. Robert M. Russell mu JAMA ya June 19, 1996. “Ndipotu kunenepa pang’ono kwa munthu wokalamba kungakhale kopindulitsa popeza kumasunga nyonga yogwiritsira ntchito atadwala ndi kuthandizira minofu ndi mafupa kukhala yolimba.”