Mawu a M'munsi
d Kufufuza kwaposachedwa kwasonyeza kuti kuphatikiza mkaka wa m’botolo ndi mkaka wa m’maŵere kungakulitse tsoka lakutenga kachilombo ka HIV ndipo kuti mkaka wa m’maŵere ungathe kukhala ndi mankhwala amene angathe kufoketsa kachilomboko. Ngati zimenezi zili zoona ndiye kuti chosankha chabwino chingakhale kuyamwitsa mkaka wa m’maŵere koma mosamala, ngakhale kuti njirayi ili n’zovuta zina. Komabe, pakali pano palibe umboni wonse wotsimikizira kufufuza kumeneku.