Mawu a M'munsi
a Galamukani! si magazini ya zamankhwala, ndipo nkhani za matenda a MCS sizinalembedwe n’cholinga chofuna kuchilikiza chithandizo cha mtundu winawake. Nkhanizi zikungofotokoza za njira zimene zatulukiridwa posachedwapa komanso njira zimene madokotala ena komanso anthu odwala matendaŵa aona kuti ndi zothandiza polimbana ndi matendaŵa. Galamukani! ikudziŵa kuti madokotala sagwirizana pankhani ya gwero la MCS, mmene matendaŵa amakhalira, kapena chithandizo ndiponso ndondomeko zambirimbiri zoperekedwa ndiponso zogwiritsidwa ntchito ndi odwala.