Mawu a M'munsi
b Chitsanzo chodziŵika bwino kwambiri cha vuto la ma enzyme ndi cha enzyme yotchedwa lactase. Anthu amene ali ndi vuto la lactase, matupi awo satha kugaya lactose wa mu mkaka, ndipo amadwala akamwa mkaka. Anthu ena alibe enzyme yokwanira yogaya tyramine, mankhwala amene amapezeka mu tchizi ndi m’zakudya zina. Choncho, anthu ameneŵa akadya zakudya za mtundu umenewo akhoza kudwala litsipa mwapafupipafupi.