Mawu a M'munsi
c Anthu amene akukhulupirira kuti akudwala MCS ayenera kupita kwa dokotala wodziŵika bwino kuti apeze chithandizo choyenera. Kungakhale kupanda nzeru kusinthiratu zochita zanu zambiri, komwe mwinanso kungawonongetse ndalama zambiri, musanayezedwe mokwanira. Mwina atakupimani angapeze kuti muyenera kusintha zakudya kapena makhalidwe anu pang’ono chabe kuti muchepetse kapenanso kuthetseratu matendawo.