Mawu a M'munsi
a Pali kusiyana kooneka bwino lomwe pakati pa mphini zotemedwa ndi cholinga chopaka mankhwala kapenanso kudzikongoletsa ndi kudzicheka mochititsa nthumanzi kapena kudula ziwalo komwe achinyamata ambiri, makamaka asungwana osakwana zaka makumi aŵiri akuchita. Kudzitema kotereku nthaŵi zambiri kumakhala chizindikiro cha kupsinjika maganizo kapena kuchitiridwa nkhanza ndipo n’kofunika thandizo la madokotala.