Mawu a M'munsi
a Mwachitsanzo, akuti buku lina lolongosola zamankhwala la m’zaka za zana loyamba lolembedwa ndi Dioscorides, linanena kuti njira yochiritsira matenda a chikasu ndiyo kumwa mankhwala opangidwa ndi vinyo osakanizidwa ndi ndoŵe zambuzi! N’zoona kuti masiku ano timadziŵa kuti mankhwala otereŵa ankangowonjezera matenda a wodwalayo.