Mawu a M'munsi
a Mawu akuti “zida zazing’ono” akutanthauza mfuti wamba ndi mfuti zoombera ndi dzanja limodzi. Izi ndi zida zimene zingathe kunyamulidwa ndi munthu mmodzi. Mawu akuti “zida zonyamulika” akutanthauza zida monga mfuti zowomba zipolopolo mosadukiza, mfuti zoponya mabomba, ndiponso zoponya mizinga, zimene nthaŵi zina zimaomberedwa ndi anthu aŵiri.