Mawu a M'munsi
a Malingaliro a anthu pankhani ya uchigaŵenga ndi osiyanasiyana kwambiri. Mwachitsanzo, m’mayiko ogaŵikana ndi nkhondo yapachiŵeniŵeni, ziwawa zochitidwa ndi gulu lina polimbana ndi gulu linzake anthu angazione ngati nkhondo yoyenera kapena monga uchigaŵenga, malinga ndi gulu lomwe lafunsidwalo. M’nkhani zino, mawu oti “uchigaŵenga” kwakukulukulu akunena za kuchita ziwawa n’cholinga choumiriza kuti pachitike chinachake.