Mawu a M'munsi
a Mboni za Yehova zimaona ntchito yawo yolalikira monga mmene mtumwi Paulo ankaionera, monga chinthu chofunikira kwa Akristu oona. Paulo anati: “Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho [“pakuti ndimafunikira kutero,” NW].” (1 Akorinto 9:16) Komabe ntchito yawo yolalikira ndi yongodzipereka chifukwa anasankha okha kukhala ophunzira a Kristu, ndipo amakhala akudziŵa bwinobwino ntchito imene ayenera kuchita akapeza mwayi umenewu.