Mawu a M'munsi
a N’kutheka kuti Samhain si dzina la mulungu wa imfa wa anthu a chi Celt monga mmene anthu ambiri amanenera, koma ndi dzina la chikondwererochi. Malingana n’zimene ananena Jean Markale, akuti amene ali katswiri wa ku France wa mbiri ya a Celt, mwina Lug, mulungu wa kuwala, ndi yemwe anali kulemekezedwa pa chikondwerero cha Samhain.