Mawu a M'munsi
a Baibulo limati pali “Harmagedo,” imene imatchedwanso kuti “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” Imeneyi si nkhondo ya anthu ayi, koma ndi nkhondo yochita kusankha imene Mulungu adzawonongere anthu ochita zoipa okha. Motero anthu sayenera kuganiza kuti chifukwa chakuti kuli Harmagedo ndiye kuti nkhondo zamasiku ano n’zabwinonso kapena kuti Mulungu amadalitsa nkhondozi.—Chivumbulutso 16:14, 16; 21:8.