Mawu a M'munsi
b Azibusa ena oganiza mopereŵera ankanena kuti malonda ogulitsa anthu mwankhanzaŵa Mulungu anali kugwirizana nawo. Motero, anthu ambiri amakhalabe ndi maganizo olakwika ameneŵa oti Baibulo limati palibe cholakwika ndi nkhanza zoterozo koma pamene ilo silitero. Chonde onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Kodi Mulungu Ankakondwera ndi Malonda a Ukapolo?” mu Galamukani! ya September 8, 2001.