Mawu a M'munsi
b Mkanda wa Baily umachitika chifukwa cha kuŵala kwa dzuŵa kukamadutsa m’zigwa za mwezi dzuŵalo lisanabisike lonse. Mawu akuti “mphete ya diamondi” amafotokoza mmene dzuŵa limaonekera likangotsala pang’ono kuti libisike lonse, pamene kachigawo kakang’ono ka dzuŵa kamakhala kakuwonekabe, zomwe zimaoneka ngati mphete yoyera yonyezimira, monga momwe mphete ya diamondi imaonekera.