Mawu a M'munsi
b Kwa nthaŵi yaitali ndithu, Akristu a Chiyuda a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino omwe anali ku Yerusalemu ankasunga mbali zosiyanasiyana za Chilamulo cha Mose, mwina chifukwa chakuti: Chilamulocho chinali chochokera kwa Yehova. (Aroma 7:12, 14) Chinali chitawaloŵerera kwambiri anthu a Chiyuda n’kungosanduka mwambo wawo. (Machitidwe 21:20) Chinali lamulo lokhazikitsidwa ndi boma, ndipo aliyense wotsutsa chilamulocho akanangochititsa kuti uthenga wachikristu utsutsidwe.