Mawu a M'munsi
a Ena mwa mavuto ameneĊµa ndi matenda a mtima, ofa ziwalo, a impso ndi matenda a mitsempha ya magazi ndi ya ubongo. Magazi akamafika ochepa ku miyendo mwendowo ungathe kutuluka zilonda, ndipo zilondazi zikanyanya amatha kungodula mwendo wonsewo. Matenda a shuga ndi amenenso amayambitsa khungu pakati pa anthu ambiri aakulu.