Mawu a M'munsi
a Kugodomala maganizo kumene tikunena m’nkhani ino kumam’chititsa munthu kukhala ngati ali mtulo ndipo nthaŵi zambiri ndi munthu wina amam’chititsa kutero. Ndipo zikatero wogodomalayo amatha kukumbukira zinthu zomwe anaziiwala kalekale, kuona zideruderu, ndipo amatha kuchita chilichonse chomwe munthu wam’godomalitsayo wamuuza kuchita.