Mawu a M'munsi
a Mu nkhanizi, Galamukani! ikufotokoza maganizo akatswiri otchuka pa zakaleredwe ka ana, popeza kuti zimene amapeza pa nkhani zoterezi akachita kafukufuku zimatha kuthandiza makolo ndi kuwadziŵitsa zina ndi zina. Komabe, n’zoona kuti zimene ofufuzaŵa amapeza kaŵirikaŵiri amadzaziunikanso n’kusintha kunena zina. Koma si choncho ndi mfundo za m’Baibulo zimene Galamukani! imagwirizana nazo kwathunthu.