Mawu a M'munsi
a Anthu ophunzira kwambiri ndiponso asayansi otchuka amene anena poyera kuti amakhulupirira zoti pali “Wokonza Zinthu Wanzeru” ndi anthu monga Phillip E. Johnson amene amaphunzitsa za malamulo pa yunivesite ya ku California, Berkeley; katswiri wa zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo Michael J. Behe, amene analemba buku lakuti Darwin’s Black Box—The Biochemical Challenge to Evolution; katswiri wa masamu William A. Dembski; katswiri wa kaganizidwe ka anthu Alvin Plantinga; akatswiri a sayansi ya kapangidwe ka zinthu John Polkinghorne ndi Freeman Dyson; katswiri wa sayansi ya zakuthambo Allan Sandage; ndi ena ambiri oti sitingakwanitse kuwatchula onse.