Mawu a M'munsi
a Buku lotchedwa The Medical Journal of Australia limati “kuda nkhaŵa ndi maonekedwe ako ndi chizindikiro chofala cha matenda angapo a maganizo.” Matendaŵa ndi monga kuvutika maganizo, kulephera kudziletsa kuchita zinthu zinazake, ndi kuvutika kudya poopa kunenepa. Choncho matenda oda nkhaŵa kwambiri ndi maonekedwe a munthu angakhale ovuta kuwatulukira.