Mawu a M'munsi
a Anita Elberse, pulofesa wa pa yunivesite inayake yotchuka ku United States (Harvard Business School), anati: “Ngakhale kuti masiku ano mafilimu nthawi zambiri amapanga ndalama zambiri kunja kwa dziko la United States kusiyana ndi zomwe amapanga m’dzikolo, ndalama zomwe filimu yapanga ku United States ndi chizindikiro chofunikabe kwambiri cha momwe malonda ake ayendere kunja.”