Mawu a M'munsi
a Moyo wongokhala ungachititse munthu kudwala matenda ena oopsa kwambiri. Mwachitsanzo, malinga ndi zimene ananena a American Heart Association, moyo woterewu, “ungachititse munthu kudwala matenda a mtima ndiponso ungachititse kuti BP izikwera. Ungachititsenso kuti munthu amwalire mosavuta chifukwa chakuti mtima ndi mitsempha ya magazi sizikugwira ntchito bwino ndiponso chifukwa cha sitiroko.”