Mawu a M'munsi
a Anthu amene angawafunse za inu akhoza kukhala mphunzitsi amene amakudziwani bwino kapena munthu amene amadziwana ndi banja lanu amene ali ndi bizinesi yake. Pouza abwanawo kuti mungawapatse mayinawo atawafuna, mungadziwe msanga ngati akufuna kukulembani ntchito. Muonetsetse kuti muyambe kaye mwawapempha anthu amene mukufuna kuti adzanene za inuwo.