Mawu a M'munsi
a Merengue ndi chamba cha nyimbo zovina mofulumira. Kale, oimba nyimbo za merengue ankakhala gulu la anthu ochepa ndipo ankaimbira zida zosiyanasiyana. Patapita nthawi, anayamba kupanga magulu a anthu ambiri. Masiku ano, magulu ambiri a merengue amaimba nyimbo zawozo pogwiritsa ntchito malipenga, ng’oma, ndi zida zina.