Mawu a M'munsi
c Pali malo ena ochezera pa Intaneti amene amati ndi a anthu akuluakulu okhaokha ndipo salola munthu wa zaka zochepa kupita pa malo amenewo. Izi zili choncho chifukwa nthawi zambiri, nkhani zake ndiponso zithunzi zimene amatumizirana zimakhala zolaula. Komabe, kafukufuku akusonyeza kuti achinyamata aang’ono kwambiri mpaka azaka naini amanama kuti ali ndi zaka zambiri pofuna kuti apeze chilolezo choti azitha kugwiritsa nawo ntchito malo ochezera a anthu akuluakulu.