Mawu a M'munsi
d Nthawi zambiri, mowa wokwana magalamu seveni umachoka m’thupi pa ola lililonse. Kukula kwa botolo kapena tambula ya mowa kumasiyanasiyana malinga ndi dziko limene muli. A bungwe la World Health Organization amati m’mayiko ambiri, botolo limodzi kapena tambula imodzi ya mowa imakhala ndi mphamvu yoledzeretsa yokwana magalamu 10. Mlingo umenewu umapezeka mu mowa wamba wochuluka mamililita 250, vinyo wochuluka mamililita 100, kapena mowa wa m’gulu la kachasu wochuluka mamililita 30.