Mawu a M'munsi
b Kuli zipatala ndiponso mabungwe ambirimbiri amene angakuthandizeni. Mboni za Yehova sizilangiza anthu kuti atsatire njira yakutiyakuti yolandirira thandizo. M’pofunika kusamala kuti munthu asadzilowetse mu zochitika zimene zili zosemphana ndi mfundo za m’Malemba. Aliyense ayenera kudzisankhira yekha thandizo limene angafunikire akaganizira mfundo zonse zofunika.