Mawu a M'munsi
a M’chaka cha 711 C.E., asilikali a Aarabu ndi a anthu ena otchedwa a Berber analowa m’dziko la Spain, ndipo pasanathe zaka seveni mbali yaikulu ya dzikoli inakhala m’manja mwa Asilamu. Pomatha zaka 200 chilowereni asilikali aja, mzinda wa Córdoba unakhala mzinda waukulu kwambiri ku Ulaya ndiponso wotsogola kwambiri pa zachikhalidwe.