Mawu a M'munsi
a Anthu ena amanena kuti zaka zotchulidwa mu nkhani ya m’Baibulo imeneyi kwenikweni ndi miyezi. Komabe, nkhaniyo imati Aripakasadi anabereka Sela ali ndi zaka 35. Ngati zimenezi zikutanthauza miyezi 35, ndiye kuti Aripakasadi anakhala tate asanakwanitse zaka zitatu, zomwe mwachidziwikire n’zosatheka. Ndiponso, machaputala oyambirira a Genesis amasiyanitsa zaka, zomwe zimayendera dzuwa, ndi miyezi, yomwe imayendera mwezi.—Genesis 1:14-16; 7:11.